Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 11:38 - Buku Lopatulika

38 Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa Iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa Iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Yesu adavutikanso mu mtima, nakafika ku manda amene anali phanga. Pakhomo pake panali chimwala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Yesu atakhudzidwanso kwambiri anafika ku manda. Manda akewo anali phanga ndipo anatsekapo ndi mwala.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 11:38
12 Mawu Ofanana  

Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wake m'phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamure (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani.


Uchitanji iwe kuno, ndimo ndani ali nawe kuno, kuti iwe wagoba manda kuno, ndi kudzigobera manda pamwamba, ndi kudzisemera mogonamo m'thanthwe.


Koma wobadwa ndi munthu iwe, usa moyo, ndi kuduka msana, ndi kuwawa mtima, uuse moyo pamaso pao.


Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mzinda, pakati pa Yerusalemu, nulembe chizindikiro pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.


nauika m'manda ake atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo.


Ndipo iwo anamuka, nasunga manda, nasindikizapo chizindikiro pamwalapo, iwo pamodzi ndi alondawo.


Ndipo anagula bafuta, namtsitsa Iye, namkulunga m'bafutamo, namuika m'manda osemedwa m'thanthwe; nakunkhunizira mwala pakhomo la manda.


Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno!


Ndipo anapeza mwala unakunkhunizidwa kuuchotsa pamanda.


Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini,


Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Maria wa Magadala mamawa, kusanayambe kucha, kumanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa