Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 11:27 - Buku Lopatulika

27 Ananena ndi Iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ananena ndi Iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Iye adati, “Inde Ambuye, ndikukhulupirira kuti Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, amene adayenera kubwera pansi pano.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Marita anamuwuza Iye kuti, “Inde Ambuye, ine ndikukhulupirira kuti ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene abwera mʼdziko lapansi.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 11:27
17 Mawu Ofanana  

Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?


Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.


Pamenepo analamulira ophunzira kuti asauze munthu kuti Iye ndiye Khristu.


pakuti wakubadwirani inu lero, m'mzinda wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye.


Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele.


ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.


Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.


Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.


Ndipo monga anapita panjira pao, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?


Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.


Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa