Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 10:20 - Buku Lopatulika

20 Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi chiwanda, nachita misala; mukumva Iye bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi chiwanda, nachita misala; mukumva Iye bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Ambiri mwa iwo ankati, “Ali ndi mizimu yoipa, ndipo wapenga. Bwanji mukumumveranso Iyeyu?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Ambiri a iwo anati, “Iye ndi wogwidwa ndi ziwanda ndi wamisala. Chifukwa chiyani mukumvera Iye?”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 10:20
15 Mawu Ofanana  

Anachotsedwa ku chipsinjo ndi chiweruziro; ndipo ndani adzafotokoza nthawi ya moyo wake? Pakuti walikhidwa kunja kuno; chifukwa cha kulakwa kwa anthu anga Iye anakhomedwa.


Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'goli.


Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamutcha mwini banja Belezebulu, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake?


Pakuti Yohane anadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, Ali ndi chiwanda.


Koma Afarisi analinkunena, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda.


Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka.


Khamu la anthu linayankha, Muli ndi chiwanda: afuna ndani kukuphani Inu?


Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa kunthawi yonse.


Koma pakudzikanira momwemo, Fesito anati ndi mau aakulu, Uli wamisala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakuchititsa misala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa