Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 10:12 - Buku Lopatulika

12 Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa sizili zake za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa sizili zake za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Koma wolembedwa ntchito chabe akaona mmbulu ulikudza, amazisiya nkhosazo iye nkuthaŵa. Amatero popeza kuti si mbusa weniweni, ndipo nkhosa si zake ai. Tsono mmbulu uja umagwirapo zina, zina nkumwazikana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Wantchito ndi mʼbusa amene nkhosazo si zake. Choncho, pamene aona mmbulu ukubwera, iye amazisiya nkhosazo ndi kuthawa. Ndipo mmbulu umagwira nkhosazo ndikuzibalalitsa.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 10:12
15 Mawu Ofanana  

Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa.


chifukwa ali wolipidwa, ndipo sasamala nkhosa.


Koma iye wakulowera pakhomo, ndiye mbusa wa nkhosa.


Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mau ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina ao, nazitsogolera kunja.


Ndidziwa ine kuti, nditachoka ine, adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo;


wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba chuma;


Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a chisiriro chonyansa;


pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya.


Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa;


Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;


Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa