Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 8:4 - Buku Lopatulika

4 Ndiponso udzati kwa iwo, Atero Yehova, Kodi adzagwa, osaukanso? Kodi wina adzachoka, osabweranso?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndiponso udzati kwa iwo, Atero Yehova, Kodi adzagwa, osaukanso? Kodi wina adzachoka, osabweranso?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Chauta adandiwuza kuti ndifunse anthu ake mau aŵa: “Kodi anthu akagwa, ndiye kuti sangathe kudzukanso? Kodi munthu akasokera, ndiye kuti sangathe kubwereranso?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 “Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti: “ ‘Kodi anthu akagwa sangadzukenso? Munthu akasochera kodi sangathe kubwereranso?

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 8:4
15 Mawu Ofanana  

tsono pempho ndi pembedzero lililonse akalipempha munthu aliyense, kapena anthu anu onse Aisraele, pakuzindikira munthu yense chinthenda cha mtima wa iye yekha, ndi kutambasulira manja ake kunyumba ino;


Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso; koma oipa akhumudwa pomfikira tsoka.


Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.


woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.


Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu choopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ochita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zake; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora.


Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.


Bwerani, ana inu obwerera, ndidzachiritsa mabwerero anu. Taonani, tadza kwa Inu; pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.


Kapena nyumba ya Yuda idzamva choipa chonse chimene nditi ndidzawachitire; kuti abwerere yense kuleka njira yake yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi tchimo lao.


Ngati udzabwera, Israele, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzachotsa zonyansa zako pamaso panga sudzachotsedwa.


Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? Ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yake, ndi kukhala ndi moyo?


Israele, bwerera kunka kwa Yehova Mulungu wako; pakuti wagwa mwa mphulupulu yako.


Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.


Ndipo kudzikuza kwa Israele kumchitira umboni pamaso pake; koma sanabwerere kunka kwa Yehova Mulungu wao, kapena kumfunafuna mwa ichi chonse.


Namwali wa Israele wagwa, sadzaukanso; wagwetsedwa pa nthaka yake, palibe womuutsa.


Usandiseka, mdani wangawe; pakugwa ine ndidzaukanso; pokhala ine mumdima Yehova adzakhala kuunika kwanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa