Yeremiya 8:16 - Buku Lopatulika16 Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mzinda ndi amene akhalamo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mudzi ndi amene akhalamo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 “Adani athu aloŵa kale mu mzinda wa Dani. Dziko lonse likunjenjemera ndi kulira kwa akavalo ao. Adani akubwera kudzaononga dzikoli pamodzi ndi zinthu zake zonse. Adzaononganso mzinda ndi onse okhalamo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Kulira kwa ngʼombe zazimuna za mdani kukumveka kuchokera ku Dani; dziko lonse likunjenjemera chifukwa cha kulira kwa akavalowo. Akubwera kudzawononga dziko ndi zonse zimene zili mʼmenemo. Adzawononga mzinda ndi onse okhalamo.” Onani mutuwo |