Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 8:15 - Buku Lopatulika

15 Tinayang'anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Tinayang'anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Tinkafuna mtendere, koma zinthu sizidatiyendere bwino. Tinkafuna kuchira, koma tidangopeza zoopsa zokhazokha.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Tinkayembekezera mtendere koma palibe chabwino chomwe chinachitika, tinkayembekezera kuchira koma tinakumana ndi zoopsa zokhazokha.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 8:15
9 Mawu Ofanana  

Muja ndinayembekeza chokoma chinadza choipa, ndipo polindira kuunika unadza mdima.


Akufunkha afika pa mapiri oti see m'chipululu; pakuti lupanga la Yehova lilusa kuyambira pa mbali ina ya dziko kufikira kumbali ina; palibe thupi lokhala ndi mtendere.


Kodi mwakanadi Yuda? Kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? Bwanji mwatipanda ife, ndipo tilibe kuchira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakuchira, ndipo taonani mantha!


Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! Ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.


Usatulukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse.


Ndipo analipoletsa pang'ono bala la mwana wamkazi wa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, mtendere; posakhala mtendere.


Chionongeko chilinkudza, adzafunafuna mtendere, koma palibe.


Pakuti wokhala mu Maroti alindira chokoma, popeza choipa chatsika kwa Yehova kunka kuchipata cha Yerusalemu.


Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa