Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 6:7 - Buku Lopatulika

7 Monga kasupe atulutsa madzi ake, chomwecho atulutsa zoipa zake; chiwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwake; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Monga kasupe atulutsa madzi ake, chomwecho atulutsa zoipa zake; chiwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwake; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Monga momwe chitsime chimasungira madzi ake, ndimonso m'mene mzindawo umasungira zoipa zake. Zimene mukumva ndi za chiwonongeko ndi za nkhondo. Ndikuwonamonso matenda ndi zilonda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Monga momwe chitsime chimatulutsira madzi ndi mmenenso Yerusalemu amatulutsira zoyipa zake. Chiwawa ndi chiwonongeko ndi zomwe zimamveka mu mzindamo; nthenda yake ndi mabala ake ndimaziona nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 6:7
24 Mawu Ofanana  

Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.


Kuchokera pansi pa phazi kufikira kumutu m'menemo mulibe changwiro; koma mabala, ndi mikwingwirima, ndi zilonda; sizinapole, ngakhale kumangidwa, ngakhale kupakidwa mafuta.


Koma oipa ali ofanana ndi nyanja yowinduka; pakuti siingapume, ndi madzi ake autsa matope ndi uve.


Maukonde ao sadzakhala zovala, sadzafunda ntchito zao; ntchito zao zili ntchito zoipa, ndi chiwawa chili m'manja mwao.


Pakuti paliponse ndinena, ndifuula; ndifuula, Chiwawa ndi chofunkha; pakuti mau a Yehova ayesedwa kwa ine chitonzo, ndi choseketsa, dzuwa lonse.


Pakuti atero Yehova, Kulaswa kwako kuli kosapoleka ndi bala lako lili lowawa.


Palibe amene adzanenera mlandu wako, ulibe mankhwala akumanga nao bala lako.


Chifukwa chanji ulirira bala lako? Kuphwetekwa kwako kuli kosapoleka; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka, ndakuchitira iwe izi.


Pakuti mzinda uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiuchotse pamaso panga;


Kodi mulibe vunguti mu Giliyadi? Kodi mulibe sing'anga m'menemo; analekeranji kuchira mwana wamkazi wa anthu anga?


Akuonera zopanda pake, akuombezera mabodza, lupanga likugoneka pa makosi a oipa olasidwa, amene lafika tsiku lao nthawi ya mphulupulu yotsiriza.


Pakuti mwazi wake uli m'kati mwake anauika pathanthwe poyera, sanautsanulire panthaka kuukwirira ndi fumbi.


Atero Ambuye Yehova, Likufikireni akalonga a Israele inu, lekani kuchita chiwawa, ndi kulanda za eni ake; muchite chiweruzo ndi chilungamo; lekani kupirikitsa anthu anga m'zolowa zao, ati Ambuye Yehova.


Chiwawa chauka chikhale ndodo ya choipa; sadzawatsalira ndi mmodzi yense, kapena wa unyinji wao, kapena wa chuma chao; sipadzakhalanso kuwalira maliro.


Sula unyolo, popeza dziko ladzala ndi milandu yamwazi, ndi mzinda wadzala ndi chiwawa.


Tsoka uyo wopanduka, ndi wodetsedwa, ndiye mzinda wozunza!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa