Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 6:2 - Buku Lopatulika

2 Ndidzachotsa mwana wamkazi wa Ziyoni mkazi wokoma ndi wololopoka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndidzachotsa mwana wamkazi wa Ziyoni mkazi wokoma ndi wololopoka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndidzauwononga mzinda wa Ziyoni, mzinda wooneka bwino ndi wokongola.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Kodi mzinda wa Ziyoni suli ngati msipu wokongola kwambiri, kumene abusa amafikako ndi ziweto zawo?

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 6:2
7 Mawu Ofanana  

Ndipo mwana wamkazi wa Ziyoni wasiyidwa ngati chitando cha m'munda wampesa, chilindo cha m'munda waminkhaka, ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.


Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.


Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba kukoma kwake kwa Israele; osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.


Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?


Omwe anadya zolongosoka angosiyidwa m'makwalala; omwe analeredwa navekedwa mlangali afungatira madzala.


Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lake popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lake lidzamuipira mwamuna wa pamtima pake, ndi mwana wake wamwamuna ndi wamkazi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa