Yeremiya 6:1 - Buku Lopatulika1 Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga mu Tekowa, kwezani chizindikiro mu Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga m'Tekowa, kwezani chizindikiro m'Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Inu anthu a ku Benjamini thaŵani, tulukanimo m'Yerusalemu. Lizani lipenga ku Tekowa, kwezani mbendera ku Betehakeremu. Tsoka likudzakugwerani kuchokera kumpoto, ndipotu nchiwonongeko chachikulu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 “Thawani, inu anthu a ku Benjamini! Tulukani mu Yerusalemu! Lizani lipenga ku Tekowa! Kwezani mbendera ku Beti-Hakeremu! Pakuti tsoka lalikulu likubwera kuchokera kumpoto, ndipo chiwonongekocho nʼchachikulu. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.