Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 51:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo ndidzatuma ku Babiloni alendo, amene adzampeta iye, amene adzataya zonse m'dziko lake, pakuti tsiku la chisauko adzamenyana ndi iye pomzungulira pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo ndidzatuma ku Babiloni alendo, amene adzampeta iye, amene adzataya zonse m'dziko lake, pakuti tsiku la chisauko adzamenyana ndi iye pomzungulira pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndidzatuma alendo ku Babiloni, kuti adzampepete ndi kuseseratu zonse zokhala m'dziko lake. Iwowo adzamuukira pa mbali zonse nthaŵi ya zoopsayo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndidzatuma alendo ku Babuloni kudzamupeta ndi kuwononga dziko lake kotheratu. Iwo adzalimbana naye ku mbali zonse pa tsiku la masautso ake.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:2
9 Mawu Ofanana  

Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele.


Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israele: Chifukwa cha inu ndatumiza ku Babiloni, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Ababiloni m'ngalawa za kukondwa kwao.


Ndawapeta ndi chopetera m'zipata za dziko; ndachotsa ana ao, ndasakaza anthu anga; sanabwerere kuleka njira zao.


Memezani amauta amenyane ndi Babiloni, onse amene akoka uta; mummangire iye zithando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wake yense; mumbwezere iye monga mwa ntchito yake; monga mwa zonse wazichita, mumchitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israele.


Ndipo wonyadayo adzakhumudwa nadzagwa, ndipo palibe amene adzamuutsa iye; ndipo Ine ndidzayatsa moto m'mizinda yake, ndipo udzatentha onse akumzungulira iye.


Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.


chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa