Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 5:7 - Buku Lopatulika

7 Bwanji ndidzakhululukira iwe? Pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anachita chigololo, nasonkhana pamodzi m'nyumba za adama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Bwanji ndidzakhululukira iwe? Pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anachita chigololo, nasonkhana masonkhano m'nyumba za adama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Chauta akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji pa zonsezi? Ana anu adandisiya Ine, ndipo adapembedza milungu imene siili milungu konse. Ine ndidaŵapatsa zonse zimene ankasoŵa, komabe adakonda kumachita chigololo, namapita ku nyumba za akazi adama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yehova akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji ndi zimene mwachita? Ana anu andisiya Ine ndipo amapembedza milungu imene si milungu konse. Ine ndinawapatsa zonse zimene ankasowa, komabe iwo anachita chigololo namasonkhana ku nyumba za akazi achiwerewere.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 5:7
39 Mawu Ofanana  

Simunapirikitse kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amachita anthu a m'maiko ena? Kuti aliyense wakudza kudzipatulira ndi mwanawang'ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu.


Pakuti ndicho moto wakunyeka mpaka chionongeko, ndi chakuzula zipatso zanga zonse.


Pakuona mbala, uvomerezana nayo, nuchita nao achigololo.


Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira pali Baala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga.


Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?


Pamenepo uziti kwa iwo, Chifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu ina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga chilamulo changa;


Kodi munthu adzadzipangira yekha milungu, imene siili milungu?


Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula.


Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israele chipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Chifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?


Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino.


Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, cholowa chabwino cha makamu a mitundu ya anthu? Ndipo ndinati mudzanditcha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine.


Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamchotsa Israele wobwerera m'mbuyo, ndi kumpatsa kalata yachilekaniro chifukwa cha kuchita chigololo iye, mphwake Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nachita dama.


Kodi mudzapha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo, ndi kulumbira zonama, ndi kupereka nsembe kwa Baala, ndi kutsata milungu ina imene simunaidziwa,


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Ha, ndikadakhala ndi chigono cha anthu aulendo m'chipululu; kuti ndisiye anthu anga, ndiwachokere, pakuti onse ali achigololo, msonkhano wa anthu achiwembu.


Ife tilakwa ndi kupikisana nanu, ndipo Inu simunatikhululukire.


Ndipo wina anachita chonyansa ndi mkazi wa mnansi wake, winanso wadetsa mpongozi wake mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wake mwana wamkazi wa atate wake.


Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.


Monga mwa podyetsa pao, momwemo anakhuta; anakhuta, ndi mtima wao unakwezeka; chifukwa chake anandiiwala Ine.


Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.


Achigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa wootcha mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo.


Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.


Iwo akulumbira ndi kutchula tchimo la Samariya, ndi kuti, Pali Mulungu wako, Dani; ndipo, Pali moyo wa njira ya ku Beereseba, iwowa adzagwa, osaukanso konse.


ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali mfumu;


Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.


Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,


Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu padziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.


Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m'chibadwidwe chao;


Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.


Anautsa nsanje yanga ndi chinthu chosati Mulungu; anautsa mkwiyo wanga ndi zopanda pake zao. Ndidzautsa nsanje yao ndi iwo osakhala mtundu wa anthu; ndidzautsa mkwiyo wao ndi mtundu wa anthu opusa.


Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.


Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.


osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kutchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa