Yeremiya 5:6 - Buku Lopatulika6 Chifukwa chake mkango wotuluka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'mizinda mwao, onse amene atulukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa zili zambiri, ndi mabwerero ao achuluka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Chifukwa chake mkango wotuluka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'midzi mwao, onse amene atulukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa zili zambiri, ndi mabwerero ao achuluka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Nchifukwa chake mkango wam'malunje udzaŵapha, mmbulu wochoka ku thengo udzaŵaononga. Kambuku adzaŵalalira pafupi ndi mizinda yao. Ndipo adzakadzula aliyense wotuluka, poti zolakwa zao nzambiri, abwereratu m'mbuyo kwambiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Choncho mkango wochokera ku nkhalango udzawapha, mmbulu wochokera ku thengo udzawawononga, kambuku adzawabisalira pafupi ndi mizinda yawo kuti akhadzule aliyense amene adzayesera kutuluka mʼmizindamo pakuti kuwukira kwawo ndi kwakukulu ndipo abwerera mʼmbuyo kwambiri. Onani mutuwo |