Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 5:18 - Buku Lopatulika

18 Koma masiku onsewo, ati Yehova, sindidzatsirizitsa konse ndi iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Koma masiku onsewo, ati Yehova, sindidzatsirizitsa konse ndi iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 “Koma ngakhale pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 “Komabe pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 5:18
10 Mawu Ofanana  

Pakuti Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi chiweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosapalamula.


Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa.


Kwerani pa makoma ake nimupasule; koma musatsirize konse; chotsani nthambi zake pakuti sizili za Yehova.


Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako aamuna ndi aakazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga mizinda yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.


Ndipo padzakhala pamene mudzati, Chifukwa chanji Yehova Mulungu wathu atichitira ife zonse izi? Ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko silili lanu.


Ndipo kunali, pakunenera ine, anamwalira Pelatiya mwana wa Benaya. Pamenepo ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula ndi mau aakulu, ndi kuti, Kalanga ine, Yehova Mulungu? Mudzatsiriza kodi otsala a Israele?


Koma diso langa lidawaleka osawaononga, sindinawathe onse m'chipululu.


Ndipo kunali, alimkukantha iwo, nditatsala ine, ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula, ndi kuti, Kalanga ine, Ambuye Mulungu! Kodi mudzaononga otsala onse a Israele pakutsanulira ukali wanu pa Yerusalemu?


Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa