Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 5:17 - Buku Lopatulika

17 Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako aamuna ndi aakazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga mizinda yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako aamuna ndi aakazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga midzi yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Adzakutherani zokolola zanu ndi chakudya chanu. Adzapha ana anu aamuna ndi aakazi, adzakupheraninso nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu. Adzaononga mipesa yanu ndi mikuyu yanu. Adzagwetsa mwankhondo mizinda yanu yamalinga imene mumaidalira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Adzakudyerani zokolola zanu ndi chakudya chanu, adzapha ana anu aamuna ndi aakazi; adzakupherani nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu, adzawononga mpesa wanu ndi mikuyu yanu. Ndi malupanga awo adzagwetsa mizinda yanu yotetezedwa imene mumayidalira.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 5:17
25 Mawu Ofanana  

Yehova analumbira padzanja lake lamanja, ndi mkono wake wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale chakudya cha adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira ntchito;


koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamtchera adzamumwa m'mabwalo a Kachisi wanga.


Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja ao.


Pakuti taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wachifumu wake pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa mizinda yonse ya Yuda.


Ndipo makola amtendere adzaonongeka chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.


Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali chipululu, ndipo mizinda yake yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wake woopsa.


Mkango wakwera kutuluka m'nkhalango mwake, ndipo waononga amitundu ali panjira, watuluka m'mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti mizinda yako ipasuke mulibenso wokhalamo.


Koma masiku onsewo, ati Yehova, sindidzatsirizitsa konse ndi iwe.


Israele ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampirikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asiriya; ndipo pomaliza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wathyola mafupa ake.


Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitipalamula mlandu, chifukwa iwo anachimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, chiyembekezo cha atate ao.


Kuwatha ndidzawathetsa iwo, ati Yehova, sipadzakhala mphesa pampesa, kapena nkhuyu pamkuyu, ndipo tsamba lidzafota, ndipo zinthu ndinawapatsa zidzawachokera.


Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mzinda ndi amene akhalamo.


Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti? Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mzindawu, potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.


Ambuye wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni; wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake; wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake.


chifukwa chake, mapiri inu a Israele, imvani mau a Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kunena ndi mapiri, ndi zitunda, ndi mitsinje, ndi zigwa, ndi zipululu zopasuka, ndi mizinda yamabwinja, imene yakhala chakudya ndi choseketsa amitundu otsala akuzungulira;


Ndipo ndidzapasula mipesa yake ndi mikuyu yake, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama zakuthengo zidzaidya.


Pakuti Israele waiwala Mlengi wake, namanga akachisi; ndipo Yuda wachulukitsa mizinda yamalinga; koma ndidzatumizira mizinda yake moto, nudzatha nyumba zake zazikulu.


Moto unyambita pamaso pao, ndi m'mbuyo mwao litentha lawi la moto; kumaso kwao dziko likunga munda wa Edeni, koma m'mbuyo mwao likunga chipululu chopanda kanthu; palibenso wakuwapulumuka.


ndidzachitira inu ichinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthenda yoondetsa ya m'chifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu chabe, popeza adani anu adzazidya.


Ndaononga amitundu; nsanja zao za kungodya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; mizinda yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.


Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.


Mtundu wa anthu umene simuudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi ntchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa