Yeremiya 5:19 - Buku Lopatulika19 Ndipo padzakhala pamene mudzati, Chifukwa chanji Yehova Mulungu wathu atichitira ife zonse izi? Ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko silili lanu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Ndipo padzakhala pamene mudzati, Chifukwa chanji Yehova Mulungu wathu atichitira ife zonse izi? Ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko silili lanu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Ndipo mukamafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta Mulungu wathu watichita zimenezi?’ Iwe Yeremiya uzidzayankha kuti, ‘Monga momwe mudasiyira Chauta, ndi kumatumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemonso ndimo m'mene inuyo muzidzatumikira anthu a m'dziko lachilendo.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Ndipo pamene anthu adzafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu wachita zimenezi?” Iwe udzawawuze kuti, “Monga momwe mwasiyira Ine ndi kutumikira milungu yachilendo mʼdziko mwanu, momwemonso mudzatumikira anthu a mʼdzikonso lachilendo.” Onani mutuwo |