Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 5:11 - Buku Lopatulika

11 Pakuti nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zinandichitira monyenga kwambiri, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pakuti nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zinandichitira monyenga kwambiri, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Anthu a ku Israele ndi a ku Yuda onse akhala osakhulupirika kwa Ine,” akuterotu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Nyumba ya Israeli ndi nyumba ya Yuda onse akhala osakhulupirika kotheratu kwa Ine.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 5:11
9 Mawu Ofanana  

Kuchokera ku malekezero a dziko ife tamva nyimbo zolemekeza wolungama. Koma ine ndinati, Ndaonda ine, ndaonda ine, tsoka kwa Ine! Amalonda onyenga amangonyenga; inde ogulitsa onyenga apambana kunyenga.


Inde, iwe sunamve; inde, sunadziwe; inde kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wachita mwachiwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa chibadwire.


Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?


Ndithu monga mkazi achokera mwamuna wake monyenga, chomwecho mwachita ndi Ine monyenga, inu nyumba ya Israele, ati Yehova.


Kwerani pa makoma ake nimupasule; koma musatsirize konse; chotsani nthambi zake pakuti sizili za Yehova.


Ha, ndikadakhala ndi chigono cha anthu aulendo m'chipululu; kuti ndisiye anthu anga, ndiwachokere, pakuti onse ali achigololo, msonkhano wa anthu achiwembu.


Anachita mosakhulupirika pa Yehova, pakuti anabala ana achilendo; mwezi wokhala udzawatha tsopano, pamodzi ndi maiko ao.


Koma iwo analakwira chipangano ngati Adamu, m'mene anandichitira monyenga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa