Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 48:9 - Buku Lopatulika

9 Patsani Mowabu mapiko, kuti athawe apulumuke; mizinda yake ikhale bwinja, lopanda wokhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Patsani Mowabu mapiko, kuti athawe apulumuke; midzi yake ikhale bwinja, lopanda wokhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Mowabu mchenjezeni, chifukwa posachedwa asakazika. Mizinda yake isanduka mabwinja, ikhala yopanda anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Mtsineni khutu Mowabu chifukwa adzasakazika; mizinda yake idzasanduka mabwinja, wopanda munthu wokhalamo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 48:9
8 Mawu Ofanana  

Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?


Ndipo ndinati, Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwa! Mwenzi nditauluka, ndi kukhaliratu.


Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.


Ndipo Yehova sanathe kupirirabe, chifukwa cha machitidwe anu oipa, ndi chifukwa cha zonyansa zimene munazichita; chifukwa chake dziko lanu likhala bwinja, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.


Mwana wamkazi iwe wokhala mu Ejipito, dzikonzere kunka kundende; pakuti Nofi adzakhala bwinja, nadzapsa, mulibenso wokhalamo.


Inu okhala mu Mowabu, siyani mizinda, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja chisanja chake pambali pakamwa pa dzenje.


Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao.


Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a chiombankhanga chachikulu, kuti akaulukire kuchipululu, ku mbuto yake, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa