Yeremiya 48:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo wakufunkha adzafikira pa mizinda yonse, sudzapulumuka mzinda uliwonse; chigwa chomwe chidzasakazidwa, ndipo chidikha chidzaonongedwa; monga wanena Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo wakufunkha adzafikira pa midzi yonse, sudzapulumuka mudzi uliwonse; chigwa chomwe chidzasakazidwa, ndipo chidikha chidzaonongedwa; monga wanena Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Woononga uja adzasakaza mzinda uliwonse, palibe mzinda ndi umodzi womwe umene udzapulumuke. Malo am'zigwa adzaonongeka, malo okwera nawonso adzasakazika. Zidzachitika monga momwe Chauta adanenera. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Wowononga adzabwera ndi kusakaza mzinda uliwonse, ndipo palibe mzinda umene udzapulumuke. Chigwa chidzasanduka bwinja ndipo malo athyathyathya a pamwamba pa phiri adzawonongedwa monga Yehova wayankhulira. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.