Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 41:8 - Buku Lopatulika

8 Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismaele, Musatiphe ife; pakuti tili ndi chuma chobisika m'mudzi, cha tirigu, ndi cha barele, ndi cha mafuta, ndi cha uchi. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismaele, Musatiphe ife; pakuti tili ndi chuma chobisika m'mudzi, cha tirigu, ndi cha barele, ndi cha mafuta, ndi cha uchi. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma pa gulu limenelo panali anthu khumi amene adaauza Ismaele kuti, “Ifeyo musatiphe, tili ndi tirigu, barele, mafuta, ndi uchi, zimene tidabisa m'minda.” Motero adaŵaleka osaŵaphera kumodzi ndi anzao aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma anthu khumi a gululo anawuza Ismaeli kuti, “Musatiphe! Tili ndi tirigu ndi barele, mafuta ndi uchi, zimene tabisa mʼmunda.” Choncho anawasiya ndipo sanawaphere pamodzi ndi anzawo aja.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 41:8
9 Mawu Ofanana  

Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.


Chiombolo cha moyo wa munthu ndicho chuma chake; koma wosauka samva chidzudzulo.


ndipo ndidzakupatsa iwe chuma cha mumdima, ndi zolemera zobisika za m'malo am'tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israele.


Ndipo dzenje moponyamo Ismaele mitembo yonse ya anthu amene anawapha, chifukwa cha Gedaliya, ndilo analipanga mfumu Asa chifukwa cha kuopa Baasa mfumu ya Israele, lomwelo Ismaele mwana wa Netaniya analidzaza ndi ophedwawo.


Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?


Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa