Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 41:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo panali, pamene analowa pakati pa mzinda, Ismaele mwana wa Netaniya anawapha, nawaponya pakati pa dzenje, iye ndi anthu okhala naye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo panali, pamene analowa pakati pa mudzi, Ismaele mwana wa Netaniya anawapha, nawaponya pakati pa dzenje, iye ndi anthu okhala naye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Atangofika pakati pa mudzi, Ismaele mwana wa Netaniya ndi anthu ake, adaŵapha onsewo naŵataya m'chitsime.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Atafika pakati pa mzinda, Ismaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi anthu amene anali naye anawapha anthuwo ndi kuwaponya mʼchitsime.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 41:7
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Peka mwana wa Remaliya, kazembe wake, anamchitira chiwembu, nawakantha limodzi mfumu ndi Arigobu ndi Ariye mu Samariya, m'nsanja ya kunyumba ya mfumu; pamodzi ndi iye panali amuna makumi asanu a Giliyadi; ndipo anamupha, nakhala mfumu m'malo mwake.


Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.


pakuti mapazi ao athamangira zoipa, afulumira kukhetsa mwazi.


Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati chovala cha ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira kumiyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.


Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosachimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi chipasuko zili m'njira mwao.


Akalonga ake m'kati mwake akunga mimbulu yakumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga.


miyendo yao ichita liwiro kukhetsa mwazi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa