Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 40:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babiloni, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babiloni, tsala; taona, dziko lonse lili pamaso pako; kulikonse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babiloni, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babiloni, tsala; taona, dziko lonse lili pamaso pako; kulikonse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Koma iwe Yeremiya, lero ndikukumasula maunyolo m'manjamu. Tiye ku Babiloni ngati ufuna, ndipo ndidzakusamala bwino. Koma ngati sufuna kupita, palibe kanthu. Dziko ndi lonseli monga ukuwonera, upite kumene uwona kuti nkoyenera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Koma tsopano taona, lero ndikukumasula unyolo umene unali mʼmanja mwako. Ngati ukufuna kupita nane ku Babuloni, tiye ndipo adzakusamala bwino. Koma ngati sukufuna kupita, ndiye usapite. Dziko ndi limeneli monga ukulioneramo. Uli ndi ufulu kupita kulikonse kumene ukufuna.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 40:4
8 Mawu Ofanana  

Dziko lonse silili pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere.


Ndipo Abimeleki anati, Taona dziko langa lili pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko.


Ndipo munati kwa akapolo anu, Munditengere iye, kuti ndimuone iye m'maso mwanga.


dziko la Ejipito lili pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m'dziko la Goseni; ndipo ngati udziwa anthu anzeru a mwa iwo, uwaike iwo ayang'anire ng'ombe zanga.


Ndipo mfumu idati kwa Hamani, siliva akhale wako, ndi anthu omwe; uchite nao monga momwe chikukomera.


Ndipo anati Yeremiya, Kunama kumeneko; ine sindipandukira kwa Ababiloni; koma sanamvere iye; ndipo Iriya anamgwira Yeremiya, nanka naye kwa akulu.


Wanditsekereza ndi guta, sindingatuluke; walemeretsa unyolo wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa