Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 40:3 - Buku Lopatulika

3 ndipo Yehova wachitengera, ndi kuchita monga ananena, chifukwa mwachimwira Yehova, ndi kusamvera mau ake, chifukwa chake chinthu ichi chakufikirani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 ndipo Yehova wachitengera, ndi kuchita monga ananena, chifukwa mwachimwira Yehova, ndi kusamvera mau ake, chifukwa chake chinthu ichi chakufikirani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ndipo zimenezi wazichitadi monga momwe adaanenera, chifukwa chakuti inu anthu mudachimwira Chauta, simudamumvere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ndipo tsopano Yehova wachitadi zimenezi monga mmene ananenera. Izi zonse zachitika chifukwa anthu inu munachimwira Yehova ndipo simunamumvere.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 40:3
12 Mawu Ofanana  

Koma atapumula, anabwereza kuchita choipa pamaso panu; chifukwa chake munawasiya m'dzanja la adani ao amene anachita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kufuula kwa Inu, munamva mu Mwamba ndi kuwapulumutsa kawirikawiri, monga mwa chifundo chanu;


Koma Inu ndinu wolungama mwa zonse zatigwera; pakuti mwachita zoona, koma ife tachita choipa;


Pakuti Yehova wa makamu, amene anakuoka iwe, wakunenera iwe choipa, chifukwa cha zoipa za nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda, zimene anadzichitira okha pakuutsa mkwiyo wanga m'mene anafukizira Baala.


Ndipo amitundu ambiri adzapita pa mzinda uwu, nadzati yense kwa mnzake, Yehova anatero nao mzinda waukulu uwu chifukwa ninji?


Pita, ukanene kwa Ebedemeleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taona, ndidzafikitsira mzinda uwu mau anga kuusautsa, osauchitira zabwino; ndipo adzachitidwa pamaso pako tsiku lomwelo.


Chifukwa mwafukiza, ndi chifukwa mwachimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m'chilamulo chake, ndi m'malemba ake, ndi m'mboni zake, chifukwa chake choipachi chakugwerani, monga lero lomwe.


Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitipalamula mlandu, chifukwa iwo anachimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, chiyembekezo cha atate ao.


Yehova wachita chomwe analingalira; watsiriza mau ake, amene analamulira nthawi yakale; wagwetsa osachitira chisoni; wakondweretsa adani pa iwe, wakweza nyanga ya amaliwongo ako.


Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


Pamenepo adzati, popeza analeka chipangano cha Yehova, Mulungu wa makolo ao, chimene anachita nao pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa