Yeremiya 40:5 - Buku Lopatulika5 Tsono asanabwerere iye anati, Bweratu kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, amene mfumu ya ku Babiloni inamyesa wolamulira mizinda ya Yuda, nukhale naye pakati pa anthu; kapena pita kulikonse ukuyesa koyenera kupitako. Ndipo kapitao wa alonda anampatsa iye phoso ndi mtulo, namleka amuke. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Tsono asanabwerere iye anati, Bweratu kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, amene mfumu ya ku Babiloni inamyesa wolamulira midzi ya Yuda, nukhale naye pakati pa anthu; kapena pita kulikonse ukuyesa koyenera kupitako. Ndipo kapitao wa alonda anampatsa iye phoso ndi mtulo, namleka amuke. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Ngati supita, ubwerere kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani amene mfumu ya ku Babiloni idaamsankha kuti akhale bwanamkubwa wa mizinda ya ku Yuda. Ukakhale ndi iyeyo pakati pa anthu, kapena upite kulikonse kumene ufuna.” Tsono mtsogoleri wa nkhondo uja adampatsa chakudya, nampatsanso mphatso, ndipo adamuuza kuti, “Ai, pita bwino!” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Yeremiya asanayankhe, Nebuzaradani anamuwuzanso kuti, “Ngati supita ndiye pita, ubwerere kwa Gedaliya, mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kuti akhale bwanamkubwa wa Yuda. Ukakhale naye pakati pa anthu, kapena upite kulikonse ukufuna.” Ndipo mtsogoleri uja anamupatsa Yeremiya chakudya ndi mphatso zina ndi kumulola kuti apite. Onani mutuwo |