Yeremiya 40:1 - Buku Lopatulika1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, Nebuzaradani kapitao wa alonda atammasula pa Rama, pamene anamtenga iye womangidwa m'maunyolo pamodzi ndi am'nsinga onse a Yerusalemu ndi Yuda, amene anatengedwa am'nsinga kunka nao ku Babiloni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, Nebuzaradani kapitao wa alonda atammasula pa Rama, pamene anamtenga iye womangidwa m'maunyolo pamodzi ndi am'nsinga onse a Yerusalemu ndi Yuda, amene anatengedwa am'nsinga kunka nao ku Babiloni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Chauta adalankhula ndi Yeremiya pa nthaŵi imene Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo adammasula ku Rama. Adaampeza ali womangidwa ndi unyolo pamodzi ndi am'ndende ena a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda opita nawo ku Babiloni. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Yehova anayankhula ndi Yeremiya pamene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anamasula Yeremiyayo ku Rama. Anamupeza Yeremiya ali womangidwa ndi unyolo pamodzi ndi amʼndende ena onse a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda amene ankapita nawo ku ukapolo ku Babuloni. Onani mutuwo |