Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 39:18 - Buku Lopatulika

18 Pakuti ndidzakupulumutsatu ndipo sudzagwa ndi lupanga, koma udzakhala nao moyo wako ngati chofunkha, pakuti wandikhulupirira Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pakuti ndidzakupulumutsatu ndipo sudzagwa ndi lupanga, koma udzakhala nao moyo wako ngati chofunkha, pakuti wandikhulupirira Ine, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ndithu ndidzakupulumutsa, ndipo sudzaphedwa pa nkhondo. Udzapulumuka chifukwa choti wandikhulupirira,’ ” akuterotu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ndithu ndidzakupulumutsa; sudzaphedwa pa nkhondo koma udzapulumuka, chifukwa wadalira Ine, akutero Yehova.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 39:18
19 Mawu Ofanana  

Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagiri anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anafuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira Iye.


Adzakuombola kuimfa m'njala, ndi kumphamvu ya lupanga m'nkhondo.


Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.


Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye.


Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake.


Yehova aombola moyo wa anyamata ake, ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye.


Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m'dziko, ndipo tsata choonadi.


Yehova wa makamu, wodala munthu wakukhulupirira Inu.


Pambali pako padzagwa chikwi, ndi zikwi khumi padzanja lamanja lako; sichidzakuyandikiza iwe.


Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu.


Iye amene akhala m'mzinda uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.


Yehova atero, Iye wakukhala m'mzindawu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye wakutulukira kunka kwa Ababiloni adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wake ngati chofunkha, nadzakhala ndi moyo.


Pakuti onse amene anachimwa opanda lamulo adzaonongeka opanda lamulo; ndi onse amene anachimwa podziwa lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo;


kuti ife amene tinakhulupirira Khristu kale tikayamikitse ulemerero wake.


chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa