Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 4:16 - Buku Lopatulika

16 Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira kudziko lakutali, nainenera mizinda ya Yuda mau ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira kudziko lakutali, nainenera midzi ya Yuda mau ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Akuti, “Muchenjeze mitundu ya anthu kuti mdani akubwera. Mulengeze kwa anthu a mu Yerusalemu kuti ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali, akufuula ndi kudzathira nkhondo mizinda ya Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Iwo akuti, “Fotokozani zimenezi kwa anthu a mitundu ina, lengezani zimenezi mu Yerusalemu kuti, ‘Ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali, akufuwula ndi kudzazinga mizinda ya Yuda.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 4:16
18 Mawu Ofanana  

Idzani pafupi, amitundu inu, kuti mumve; mverani anthu inu, dziko ndi zinthu zonse zotulukamo.


Ndipo anadza Yesaya mneneri kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Kodi anthu awa ananena bwanji, ndipo iwo achokera kuti, kudza kwa inu? Ndipo Hezekiya anati, Iwo achokera ku dziko lakutali, kudza kwa ine, kunena ku Babiloni.


Pakuti taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wachifumu wake pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa mizinda yonse ya Yuda.


Akulu ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzachita maliro ao, sadzadzicheka, sadzadziyeseza adazi, chifukwa cha iwo;


Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lake, mizinda yake yatenthedwa, mulibenso wokhalamo.


Tamvani mau a Yehova, amitundu inu, lalikirani m'zisumbu zakutali; ndi kuti, Iye amene anabalalitsa Israele adzasonkhanitsa, nadzamsunga, monga mbusa achita ndi zoweta zake.


Chaka chachisanu ndi chinai cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi nkhondo yake yonse ku Yerusalemu, ndi kuumangira misasa.


Monga adindo a m'munda amzinga iye; chifukwa andipandukira Ine, ati Yehova.


Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutali, inu nyumba ya Israele, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene chinenero chake simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.


Chifukwa chake mkango wotuluka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'mizinda mwao, onse amene atulukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa zili zambiri, ndi mabwerero ao achuluka.


Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babiloni wagwidwa, Beli wachitidwa manyazi, Merodaki wathyokathyoka, zosema zake zachitidwa manyazi, mafano ake athyokathyoka.


Chifukwa chake tamverani, amitundu inu, dziwani, msonkhano inu, chimene chili mwa iwo.


Tamva, dziko lapansi iwe; taona, Ine ndidzatengera choipa pa anthu awa, chipatso cha maganizo ao, pakuti sanamvere mau anga, kapena chilamulo changa, koma wachikana.


Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu uchokera kumpoto; ndi mtundu waukulu udzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi.


Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni.


Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi mu Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo?


M'dzanja lake lamanja muli ula wa ku Yerusalemu, kuika zogundira, kutsegula pakamwa pa kupha, kukweza mau ndi kufuula, kuikira zitseko zogundira, kuundira mtumbira, kumanga malinga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa