Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 4:15 - Buku Lopatulika

15 Pakuti mau anena mu Dani nalalikira nsautso m'phiri la Efuremu:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Pakuti mau anena m'Dani nalalikira nsautso m'phiri la Efuremu:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Pakuti amithenga a ku Dani akulalika mau, akulengeza zoopsa kuchokera ku Phiri la Efuremu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Pakuti amithenga akulalika mawu mʼdziko la Dani; akulengeza za masautso kuchokera ku mapiri a Efereimu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 4:15
8 Mawu Ofanana  

Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.


Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikulu lituluka m'dziko la kumpoto, likachititse mizinda ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe.


Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga mu Tekowa, kwezani chizindikiro mu Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu.


Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mzinda ndi amene akhalamo.


Ndipo Yoswa ananena nao, Ngati muli anthu aunyinji, kwerani kuli mitengoko, ndi kudziswera minda m'dziko la Aperizi ndi la Arefaimu; akakucheperani malo kuphiri la Efuremu.


Ndipo anapatula Kedesi mu Galileya ku mapiri a Nafutali, ndi Sekemu ku mapiri a Efuremu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.


Ndipo analitcha dzina la mzindawo Dani, kutsata dzina la atate wao Dani wombala Israele; koma poyambapo dzina la mzinda linali Laisi.


Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa