Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 4:11 - Buku Lopatulika

11 Pa nthawi yomweyo adzati kwa anthu awa ndi kwa Yerusalemu, Mphepo yotentha yochokera kumapiri oti see m'chipululu yopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga, yosapetera, yosayeretsa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pa nthawi yomweyo adzati kwa anthu awa ndi kwa Yerusalemu, Mphepo yotentha yochokera kumapiri oti see m'chipululu yopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga, yosapetera, yosayeretsa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Nthaŵiyo ikadzafika, anthu a mu Yerusalemu adzaŵauza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo am'chipululu ikukuntha pa anthu anga, osatitu mphepo yopetera kapena kuyeretsera zinthu ai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa;

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 4:11
28 Mawu Ofanana  

Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.


Chomwecho ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, chifukwa cha kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.


Munalimbana naye pang'ono, pamene munamchotsa; wamchotsa iye kuomba kwake kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.


Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele.


Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse zili ngati chovala chodetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo.


Chifukwa chake ndidzabalalitsa iwo, monga ziputu zakupita, ndi mphepo ya kuchipululu.


Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukulu, ndi bala lopweteka kwambiri.


Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, kwatuluka, inde chimphepo chozungulira; chidzagwa pamutu pa woipa.


mphepo yolimba yochokera kumeneko idzandifika ine; tsopanonso ndidzaweruza iwo maweruzo.


Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi mu Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo?


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzachitanji, chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu anga?


Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mzindawu.


M'diso mwanga mutsika mitsinje ya madzi chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga woonongedwa.


Manja a akazi achisoni anaphika ana aoao; anali chakudya chao poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.


Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao; koma mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga wasanduka wankhanza, ngati nthiwatiwa za m'chipululu.


Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga, ikula koposa tchimo la Sodomu, umene unapasuka m'kamphindi, anthu osauchitira kanthu.


Inde ungakhale waokedwa udzakondwa kodi? Sudzauma chiumire kodi pakuuomba mphepo ya kum'mawa? Udzauma pookedwa apo udaphuka.


Koma unazulidwa mwaukali, unaponyedwa pansi ndi mphepo ya kum'mawa, inaumitsa zipatso zake, ndodo zake zolimba zinathyoka ndi kuuma, moto unazitha.


Chinkana abala mwa abale ake, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kuchokera kuchipululu; ndi gwero lake lidzaphwa, ndi kasupe wake adzauma, adzafunkha chuma cha akatundu onse ofunika.


Chifukwa chake adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame akamuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi wotuluka kukafwambira.


Mphepo yamkulunga m'mapiko ake, ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zao.


Pamenepo adzapitirira ngati mphepo, nadzalakwa ndi kupalamula, iye amene aiyesa mphamvu yake mulungu wake.


Pakuti taonani, ndiukitsa Ababiloni, mtundu uja wowawa ndi waliwiro, wopitira pa chitando cha dziko lapansi, kulowa m'malo mosati mwao, mukhale mwaomwao.


chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.


amene chouluzira chake chili m'dzanja lake, kuti ayeretse padwale pake, ndi kusonkhanitsa tirigu m'nkhokwe yake; koma mankhusu adzatentha m'moto wosazima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa