Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 39:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m'mzinda, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am'nsinga ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m'mudzi, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am'nsinga ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo, adatenga anthu onse otsala a mumzindawo kupita nawo ku Babiloni. Ameneŵa ndiwo amene adaadzipereka kwa iye, ndiponso anthu amene adaatsalira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo a mfumu, anatenga ukapolo anthu onse otsala mu mzindamo kupita nawo ku Babuloni, pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa iye.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 39:9
20 Mawu Ofanana  

Amidiyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Ejipito kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.


Nadzatenga ena a ana ako otuluka mwa iwe, amene udzawabala, nadzakhala iwo adindo m'chinyumba cha mfumu ya Babiloni.


Ndi anthu otsalira m'mzinda, ndi opanduka akuthawira kwa mfumu ya Babiloni, ndi aunyinji otsalira, Nebuzaradani mkulu wa olindirira anamuka nao andende.


Ndipo Nebuzaradani mkulu wa olindirira anawatenga, napita nao kwa mfumu ya Babiloni ku Ribula.


Chifukwa chake anthu anga amuka m'nsinga, chifukwa cha kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi.


Pakuti atero Yehova, Taonani, ndidzaponya kunja okhala m'dziko ili tsopanoli, ndi kuwasautsa, kuti azindikire.


chifukwa chake ndidzakutulutsani inu m'dziko muno munke kudziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, kumene sindidzachitira inu chifundo.


Ndipo monga nkhuyu zoipa, zosadyeka, poti nzoipa; ntheradi atero Yehova, Chomwecho ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi akulu ake, ndi otsala a mu Yerusalemu, amene atsala m'dziko ili, ndi amene akhala m'dziko la Ejipito.


Ndipo mfumu Zedekiya anati kwa Yeremiya, Ine ndiopa Ayuda amene anandipandukira ine kunka kwa Ababiloni, angandipereke ine m'manja mwao, angandiseke.


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, Nebuzaradani kapitao wa alonda atammasula pa Rama, pamene anamtenga iye womangidwa m'maunyolo pamodzi ndi am'nsinga onse a Yerusalemu ndi Yuda, amene anatengedwa am'nsinga kunka nao ku Babiloni.


Ndipo pamene akulu onse a makamu amene anali m'minda, iwo ndi anthu ao, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni adamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu wolamulira dziko, nampatsira amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi aumphawi a m'dzikomo, a iwo amene sanatengedwe ndende kunka nao ku Babiloni;


Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga iwo, nadza nao kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula.


Ndipo mfumu ya ku Babiloni anawakantha, nawapha pa Ribula m'dziko la Hamati. Chomwecho Yuda anatengedwa ndende kutuluka m'dziko lake.


Pamenepo Daniele anabweza mau a uphungu wanzeru kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, adatulukawo kukapha eni nzeru a ku Babiloni;


Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang'ono mwa amitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa