Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 39:10 - Buku Lopatulika

10 Koma aumphawi a anthu, amene analibe kanthu, Nebuzaradani kapitao wa alonda anawasiya m'dziko la Yuda, nawapatsa mipesa ndi minda nthawi yomweyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Koma aumphawi a anthu, amene analibe kanthu, Nebuzaradani kapitao wa alonda anawasiya m'dziko la Yuda, nawapatsa mipesa ndi minda nthawi yomweyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondoyo, adasiya anthu okhaokha osauka kwambiri, ndi opanda nkanthu komwe m'dziko la Yuda. Ndipo adaŵapatsa minda yamphesa ndi minda inanso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Koma Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo anasiya mʼdziko la Yuda anthu ena osauka, amene analibe chilichonse; ndipo anawapatsa minda ya mpesa ndi minda inanso.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 39:10
8 Mawu Ofanana  

Koma mkulu wa olindirira anasiya osaukadi a m'dziko akhale osunga minda yampesa, ndi alimi.


Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti munthu adzaweta ng'ombe yaikazi yaing'ono, ndi nkhosa ziwiri;


Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Ababiloni, amene adzadza kwa ife; koma inu sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'mizinda imene mwailanda.


Ndipo pamene akulu onse a makamu amene anali m'minda, iwo ndi anthu ao, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni adamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu wolamulira dziko, nampatsira amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi aumphawi a m'dzikomo, a iwo amene sanatengedwe ndende kunka nao ku Babiloni;


ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, mwana wake wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wake wa Neriya;


Koma Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya aumphawi a padziko akhale akulima mphesa ndi akulima m'minda.


Wobadwa ndi munthu iwe, iwo okhala kumabwinja a dziko la Israele anena, ndi kuti, Abrahamu anali yekha, nakhala nalo dziko cholowa chake; koma ife ndife ambiri, dzikoli lipatsidwa kwa ife cholowa chathu.


M'mwemo ndinadyetsa zoweta zakukaphedwa, ndizo zoweta zonyankhalala. Ndipo ndinadzitengera ndodo ziwiri; ina ndinaitcha Chisomo, inzake ndinaitcha Chomanganitsa; ndipo ndinadyetsa zowetazo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa