Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 39:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo akulu onse a mfumu ya ku Babiloni analowa, nakhala m'chipata chapakati, Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu, mkulu wa adindo, Neregali-Sarezare mkulu wa alauli ndi akulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo akulu onse a mfumu ya ku Babiloni analowa, nakhala m'chipata chapakati, Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu, mkulu wa adindo, Nerigalisarezara mkulu wa alauli ndi akulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pamenepo akuluakulu onse a mfumu ya ku Babiloni adaloŵa nakakhala pa chipata chapakati. Anali aŵa: Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu mkulu wa nduna, ndi Neregali-Sarezere winanso mkulu wolamulira gulu lankhondo lapatsogolo, pamodzi ndi akuluakulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pamenepo akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni anabwera nakakhala pa Chipata Chapakati. Akuluwo ndi awa: Nerigali-Sarezeri, Samugara Nebo, Sarisekimu mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri winanso mlangizi wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 39:3
6 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu a Babiloni anapanga Sukoti-Benoti, ndi anthu a Kuta anapanga Neregali, ndi anthu a Hamati anapanga Ashima,


Pakuti taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wachifumu wake pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa mizinda yonse ya Yuda.


Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mzinda uwu.


Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Ngati mudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mzindawu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu;


Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatumiza, ndi Nebusazibani, mkulu wa adindo Rabi-Sarisi, ndi Neregali-Sarezere mkulu wa alauli, ndi akulu onse a mfumu ya ku Babiloni;


Popeza achuluka akavalo ake, fumbi lao lidzakukuta; malinga ako adzagwedezeka ndi phokoso la apakavalo, ndi njinga za magaleta, polowa iye pa zipata zako, monga umo amalowera m'mzinda popasukira linga lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa