Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 39:2 - Buku Lopatulika

2 Chaka chakhumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai, mzinda unabooledwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Chaka chakhumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai, mudzi unabooledwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Pa chaka chakhumi ndi chimodzi cha ufumu wa Zedekiya, mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai la mweziwo, malinga a mzindawo adabooledwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi wachinayi wa chaka cha khumi ndi chimodzi cha Zedekiya, malinga a mzindawo anabowoledwa.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 39:2
13 Mawu Ofanana  

Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wake wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi chimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wachisanu.


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova chaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinali chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara.


Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo kumzinda uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo.


Ndipo Ababiloni adzabweranso, nadzamenyana ndi mzinda uwu; ndipo adzaulanda, nadzautentha ndi moto.


Kwerani pa makoma ake nimupasule; koma musatsirize konse; chotsani nthambi zake pakuti sizili za Yehova.


Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chiwiri cha undende wathu, mwezi wakhumi, tsiku lachisanu la mweziwo, anandidzera wina wopulumuka ku Yerusalemu, ndi kuti, Wakanthidwa mzinda.


Nudzitengere chiwaya chachitsulo, ndi kuchiika ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo; nuulozetsere nkhope yako kuti umangidwire misasa, ndipo udzamangira misasa. Ichi chikhale chizindikiro cha nyumba ya Israele.


Limodzi la magawo ake atatu utenthe ndi moto pakati pa mzinda pakutha masiku a kuzingidwa mzinda, nutenge gawo lina ndi kukwapulakwapula ndi lupanga pozungulira pake, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.


Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira lochokera ku Chipata cha Nsomba, ndi kuchema kochokera kudera lachiwiri, ndi kugamuka kwakukulu kochokera kuzitunda.


Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa