Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 39:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa natuluka m'mzinda usiku, panjira pamunda wa mfumu, pa chipata cha pakati pa makoma awiri; ndipo iye anatulukira panjira ya kuchidikha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa natuluka m'mudzi usiku, panjira pa munda wa mfumu, pa chipata cha pakati pa makoma awiri; ndipo iye anatulukira pa njira ya kuchidikha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Pamene Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, adaŵaona, iyeyo pamodzi ndi ankhondo ake adathaŵa mumzindamo usiku, kudzera ku munda wa mfumu, kubzola pa chipata cha pakati pa zipupa ziŵiri. Adathaŵira ku Araba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Zedekiya mfumu ya Yuda pamodzi ndi ankhondo ake atawaona, anathawa mu mzindawo usiku podzera ku munda wa mfumu, kudutsa chipata cha pakati pa makoma awiri. Anathawira ku Araba.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 39:4
17 Mawu Ofanana  

Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake, nalimbitsa Milo m'mzinda wa Davide, napanga zida ndi zikopa zochuluka.


Inu munapanganso chosungamo madzi a thamanda lakale, pakati pa malinga awiri; koma inu simunamuyang'ane iye amene anachichita icho, ngakhale kusamalira iye amene analipanga kale.


Olamulira ako onse athawa pamodzi, anamangidwa ndi amauta; opezedwa ako onse anamangidwa pamodzi, nathawira patali.


pamenepo ndidzasautsa Ariyele, ndipo padzakhala maliro ndi kulira; koma iye adzakhala kwa Ine monga Ariyele.


ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m'dzanja la Ababiloni, koma adzaperekedwadi m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;


ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babiloni, ndipo adzakhala komweko kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Ababiloni, simudzapindula konse?


Kalongayo ali pakati pao adzasenza paphewa pake mumdima, nadzatuluka; adzaboola palinga, nadzatulutsapo; adzaphimba nkhope yake kuti asapenye dziko ndi maso ake.


Uzitulutsa akatundu ako usana pamaso pao, ngati a pa ulendo wa kundende; ndipo madzulo uzituluka wekha pamaso pao, monga amatuluka olowa kundende.


Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.


Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.


Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake;


Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa