Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 38:9 - Buku Lopatulika

9 Mbuyanga mfumu, anthu awa anachita zoipa m'zonse anachitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo chifukwa cha njala; pakuti mulibe chakudya china m'mzindamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Mbuyanga mfumu, anthu awa anachita zoipa m'zonse anachitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo chifukwa cha njala; pakuti mulibe chakudya china m'mudzimu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Mfumu mbuyanga, anthu aŵa amchita zoipa kwambiri mneneri Yeremiya. Amponya m'chitsime, ndipo poti buledi adatha mu mzinda, adzafa ndi njala m'menemo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Mbuye wanga mfumu, zimene anthu awa amuchitira mneneri Yeremiya ndi zoyipa kwambiri. Iwo amuponya mʼchitsime, ndipo adzafa ndi njala chifukwa buledi watha mu mzinda muno.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 38:9
12 Mawu Ofanana  

popeza ndinaopa unyinji waukulu, ndi chipepulo cha mafuko chinandiopsetsa; potero ndinakhala chete osatuluka pakhomo panga.


Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.


Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m'bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma kumseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m'mzinda. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi.


Ndipo mfumu inamuuza Ebedemeleki Mkusi, kuti, Tenga anthu makumi atatu, umkweze numtulutse Yeremiya mneneri m'dzenjemo, asanafe.


Ebedemeleki anatuluka m'nyumba ya mfumu, nanena ndi mfumu, kuti,


Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m'manja a anthu amene uwaopa.


Mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi, njala inavuta m'mzinda, ndipo anthu a m'dziko analibe zakudya.


Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate; ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao; taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.


anaononga moyo wanga m'dzenje, naponya mwala pamwamba pa ine;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa