Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 38:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo mfumu inamuuza Ebedemeleki Mkusi, kuti, Tenga anthu makumi atatu, umkweze numtulutse Yeremiya mneneri m'dzenjemo, asanafe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo mfumu inamuuza Ebedemeleki Mkusi, kuti, Tenga anthu makumi atatu, umkweze numtulutse Yeremiya mneneri m'dzenjemo, asanafe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono mfumu idalamula Mkusi Ebedemeleki kuti, “Tenga anthu atatu, mukamtulutse mneneri Yeremiya asanafe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Tsono mfumu inalamula Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, “Tenga anthu makumi atatu, ndipo mukamutulutse mʼchitsimemo mneneri Yeremiya asanafe.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 38:10
7 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pamene mfumu inaona Estere mkazi wamkuluyo alikuima m'bwalo, inamkomera mtima; ndi mfumu inamloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide inali m'dzanja lake. Nayandikira Estere, nakhudza nsonga ya ndodoyo.


Pamenepo mfumu Ahasuwero anati kwa mkazi wamkulu Estere, ndi kwa Mordekai Myuda, Taonani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndi iyeyu anampachika pamtanda, chifukwa anatulutsa dzanja lake pa Ayuda.


Ndipo ndidzatseteka nyanga zonse za oipa; koma nyanga za wolungama zidzakwezeka.


Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi; aulozetsa komwe afuna.


Ndipo Ebedemeleki anatenga anthuwo, nalowa nao m'nyumba ya mfumu ya pansi pa nyumba ya chuma, natenga m'menemo nsalu zakale zotaya ndi zansanza zovunda, nazitsitsira ndi zingwe kwa Yeremiya m'dzenjemo.


Ndipo pamene Ebedemeleki Mkusi, mdindo, anamva kuti anamuika Yeremiya m'dzenje; mfumu ilikukhala pa Chipata cha Benjamini;


Mbuyanga mfumu, anthu awa anachita zoipa m'zonse anachitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo chifukwa cha njala; pakuti mulibe chakudya china m'mzindamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa