Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 3:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamchotsa Israele wobwerera m'mbuyo, ndi kumpatsa kalata yachilekaniro chifukwa cha kuchita chigololo iye, mphwake Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nachita dama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamchotsa Israele wobwerera m'mbuyo, ndi kumpatsa kalata wachilekaniro chifukwa cha kuchita chigololo iye, mphwake Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nachita dama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Adaona kuti Israele wosakhulupirika uja ndidamsudzula ndi kumpirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda, mbale wake, sadaope. Iyenso adakhala wosakhulupirika, adapita kukachita zadama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Anaona kuti ndinasudzula Israeli wosakhulupirikayo ndi kumupirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanaope, nayenso anapita kukachita chigololo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 3:8
20 Mawu Ofanana  

Anamanganso misanje m'mapiri a Yuda, nachititsa okhala mu Yerusalemu chigololo, nakankhirako Ayuda.


Atero Yehova, Kalata ya chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.


Choipa chako chidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu.


Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.


Kodi sulingalira chomwe anena anthu awa, kuti, Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, wataya iwo? Chomwecho anyoza anthu anga, kuti asakhalenso mtundu pamaso pao.


Bwanji ndidzakhululukira iwe? Pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anachita chigololo, nasonkhana pamodzi m'nyumba za adama.


Ndi mkulu wako ndiye Samariya, wokhala kudzanja lako lamanzere, iye ndi ana ake aakazi; ndi mng'ono wako wokhala kudzanja lako lamanja ndiye Sodomu ndi ana ake aakazi.


Koma sunayende m'njira zao, kapena kuchita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kuvunda kwako, m'njira zako zonse.


Ngakhale Samariya sanachite theka la zochimwa zako, koma unachulukitsa zonyansa zako, kuwaposa iwowa, ndi kuika abale ako olungama ndi zonyansa zako zonse unazichita.


Ndipo analowa kwa iye monga umo amalowera kwa mkazi wachigololo, motero analowa kwa Ohola ndi Oholiba akazi oipawo.


Chifukwa chake ndampereka m'dzanja la mabwenzi ake, m'dzanja la Aasiriya amene anawaumirira.


Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;


Munthu akatenga mkazi akhale wake, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pake, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, amlembere kalata ya chilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lake, ndi kumtulutsa m'nyumba mwake.


Ndipo akamuda mwamuna wachiwiriyo, nakamlemberanso kalata ya chilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lake, nakamtulutsa m'nyumba mwake; kapena akamwalira mwamuna wotsirizayo, amene anamtenga akhale mkazi wake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa