Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 3:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona chimene wachichita Israele, wobwerera m'mbuyo? Wakwera pa mapiri aatali onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kuchita dama pamenepo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona chimene wachichita Israele, wobwerera m'mbuyo? Wakwera pa mapiri atali onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kuchita dama pamenepo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Pa nthaŵi ya mfumu Yosiya, Chauta adati, “Kodi waona zimene wosakhulupirika uja Israele adachita? Ankakwera kukapembedza pa phiri, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira. Motero kumeneko ankakachita zadama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Pa nthawi ya Mfumu Yosiya Yehova anandiwuza kuti, “Kodi waona zomwe Israeli wosakhulupirika uja wachita? Anakwera pa phiri lililonse lalitali ndi kupita pa tsinde pa mtengo uliwonse wogudira kukapembedza. Choncho anachita za chiwerewere kumeneko.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 3:6
24 Mawu Ofanana  

Pakuti anadzimangiranso misanje, ndi zoimiritsa, ndi zifanizo, pa chitunda chonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo wogudira uliwonse;


Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi atatu mphambu chimodzi.


Ndipo anadziipsa nazo ntchito zao, nachita chigololo nao machitidwe ao.


Koma sendererani kuno chifupi, inu ana aamuna a watsenga, mbeu yachigololo ndi yadama.


Pamwamba paphiri lalitalitali unayala mphasa yako; kumenekonso wakwera kukapereka nsembe.


amene anamdzera mau a Yehova masiku a Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Ayuda chaka chakhumi ndi chitatu cha ufumu wake.


Abwerera kuchitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu ina kuti aitumikire; nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao.


Pokumbukira ana ao maguwa a nsembe ao ndi zoimiritsa zao kumitengo yaiwisi ya pa zitunda zazitali.


Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamchotsa Israele wobwerera m'mbuyo, ndi kumpatsa kalata yachilekaniro chifukwa cha kuchita chigololo iye, mphwake Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nachita dama.


Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? Pakuti Yehova walenga chatsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.


Pakuti nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zinandichitira monyenga kwambiri, ati Yehova.


Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda mu upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo.


Pakumanga nyumba yako yachimphuli pa mphambano zilizonse, ndi pomanga chiunda chako m'makwalala ali onse, sunakhale ngati mkazi wadama waphindu, popeza unapeputsa mphotho.


Chifukwa chake, wachigololo iwe, tamvera mau a Yehova:


Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.


Pamene mng'ono wake Oholiba anachiona, anavunda ndi kuumirira kwake koposa iyeyo; ndi zigololo zake zidaposa zigololo za mkulu wake.


Ndipo maina ao ndiwo Ohola wamkulu, ndi Oholiba mng'ono wake; nakhala anga, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo maina ao, Samariya ndiye Ohola, ndi Yerusalemu ndiye Oholiba.


Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m'mbuyo kundileka Ine; chinkana akawaitana atsate Iye ali m'mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense.


Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi minjali, ndi mkundi; popeza mthunzi wake ndi wabwino, chifukwa chake ana anu aakazi achita uhule, ndi apongozi anu achita chigololo.


Koma sanamvere angakhale oweruza ao, pakuti anamuka kupembedza milungu ina, naigwadira; anapatuka msanga m'njira yoyendamo makolo ao, pomvera malamulo a Yehova; sanatero iwowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa