Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 26:2 - Buku Lopatulika

2 Yehova atero: Ima m'bwalo la nyumba ya Yehova, ndi kunena kwa mizinda yonse ya Yuda, imene imadza kudzagwadira m'nyumba ya Yehova, mau onse amene ndikuuza iwe kuti unene kwa iwo; usasiyepo mau amodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Yehova atero: Ima m'bwalo la nyumba ya Yehova, ndi kunena kwa midzi yonse ya Yuda, imene imadza kudzagwadira m'nyumba ya Yehova, mau onse amene ndikuuza iwe kuti unene kwa iwo; usasiyepo mau amodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Kaime m'bwalo la Nyumba ya Chauta. Ndipo ukalankhule kwa anthu onse okhala m'mizinda ya ku Yuda, amene amakapembedza ku Nyumba imeneyo. Ukaŵauze zonse zimene ndakulamula kuti ukanene, osasiyapo kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Kayime mʼbwalo la Nyumba ya Yehova. Ndipo ukayankhule kwa anthu onse okhala mʼmizinda ya ku Yuda amene amabwera kudzapembedza ku Nyumba ya Yehova. Ukawawuze zonse zomwe ndakulamula; usakasiyeko ndi mawu amodzi omwe.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 26:2
32 Mawu Ofanana  

Koma iwe ukwinde m'chuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao.


Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.


Pamenepo Yeremiya anadza kuchokera ku Tofeti, kumene Yehova anamtuma iye kuti anenere; ndipo anaima m'bwalo la nyumba ya Yehova, nati kwa anthu onse:


Mneneri wokhala ndi loto, anene loto lake; ndi iye amene ali ndi mau anga, anene mau anga mokhulupirika. Kodi phesi ndi chiyani polinganiza ndi tirigu? Ati Yehova.


amene mneneri Yeremiya ananena kwa anthu onse a Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu, kuti,


Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa Hananiya mneneri pamaso pa ansembe, ndi pamaso pa anthu onse amene anaima m'nyumba ya Yehova,


Ndipo Baruki anawerenga m'buku mau a Yeremiya m'nyumba ya Yehova, m'chipinda cha Gemariya mwana wa Safani mlembi, m'bwalo la kumtunda, pa khomo la Chipata Chatsopano cha nyumba ya Yehova, m'makutu a anthu onse.


Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti chilichonse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu.


Ima m'chipata cha nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova.


Ndipo uzinena kwa iwo mau awa onse, koma sadzakumvera iwe; ndipo udzawaitananso; koma sadzakuyankha iwe.


Ananenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, mau anga onse ndidzawanena ndi iwe uwalandire m'mtima mwako, utawamva m'makutu mwako.


Iwe tsono, wobadwa ndi munthu, ndakuika mlonda wa nyumba ya Israele, m'mwemo imva mau a pakamwa panga, nundichenjezere iwo.


Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m'makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israele zonse uziona.


ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Ndipo analikuphunzitsa mu Kachisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu a anthu anafunafuna kumuononga Iye;


Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi mu Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhule kanthu.


Koma mamawa anadzanso ku Kachisi, ndipo anthu onse anadza kwa Iye; ndipo m'mene anakhala pansi anawaphunzitsa.


kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba zanu,


Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.


Ndipo anadza wina nawafotokozera, kuti, Taonani, amuna aja mudawaika m'ndende ali mu Kachisi, alikuimirira ndi kuphunzitsa anthu.


Ndipo masiku onse, mu Kachisi ndi m'nyumba, sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikira Khristu Yesu.


Chilichonse ndikuuzani, muchisamalire kuchichita; musamaonjezako, kapena kuchepsako.


Koma kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mafuko anu onse kuikapo dzina lake, ndiko ku chokhalamo chake, muzifunako, ndi kufikako;


Musamaonjeza pa mau amene ndikuuzani, kapena kuchotsapo, kuti musunge malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani.


Panalibe mau amodzi a zonse adazilamulira Mose osawerenga Yoswa pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, ndi akazi ndi ana aang'ono, ndi alendo akuyenda pakati pao.


ndipo aliyense akachotsako pa mau a buku la chinenero ichi, Mulungu adzamchotsera gawo lake pa mtengo wa moyo, ndi m'mzinda woyerawo, ndi pa izi zilembedwa m'bukumu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa