Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 22:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo amitundu ambiri adzapita pa mzinda uwu, nadzati yense kwa mnzake, Yehova anatero nao mzinda waukulu uwu chifukwa ninji?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo amitundu ambiri adzapita pa mudzi uwu, nadzati yense kwa mnzake, Yehova anatero nao mudzi waukulu uwu chifukwa ninji?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 “Pamene anthu a mitundu ina adzadutse pa mzinda umenewu, azidzafunsana kuti, ‘Kodi chifukwa chiyani Chauta adaononga chotere mzinda waukuluwu?’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Pamene anthu a mitundu ina adzadutsa pa mzinda umenewu adzafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere pa mzinda waukuluwu?’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:8
13 Mawu Ofanana  

Ndipo padzakhala, pamene udzaonetsa anthu awa mau awa onse, ndipo iwo adzati kwa iwe, Chifukwa chake nchiyani kuti Yehova watinenera ife choipa chachikulu ichi? Mphulupulu yathu ndi yanji? Tchimo lathu lanji limene tachimwira Yehova Mulungu wathu?


Ndipo kapitao wa alonda anatenga Yeremiya, nati kwa iye, Yehova Mulungu wako ananenera choipa ichi malo ano;


ndipo Yehova wachitengera, ndi kuchita monga ananena, chifukwa mwachimwira Yehova, ndi kusamvera mau ake, chifukwa chake chinthu ichi chakufikirani.


Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirire, ngakhale onse okhala kunja kuno, kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m'zipata za Yerusalemu.


Koma ndidzawasiya owerengeka apulumuke lupanga, ndi njala, ndi mliri, kuti afotokoze zonyansa zao kwa amitundu kumene afikako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zochita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazichite kopanda chifukwa zonse ndinazichita momwemo, ati Ambuye Yehova.


Ndipo amitundu adzadziwa kuti nyumba ya Israele idalowa undende chifukwa cha mphulupulu zao, popeza anandilakwira Ine; ndipo ndinawabisira nkhope yanga; m'mwemo ndinawapereka m'dzanja la adani ao, nagwa iwo onse ndi lupanga.


Momwemo chidzakhala chotonza ndi mnyozo, chilangizo ndi chodabwitsa kwa amitundu akukuzinga, pamene ndikuchitira maweruzo mu mkwiyo ndi ukali ndi madzudzulo aukali; Ine Yehova ndanena.


Ambuye, chilungamo ncha Inu, koma kwa ife manyazi a nkhope yathu, monga lero lino; kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala mu Yerusalemu, ndi kwa Aisraele onse okhala pafupi ndi okhala kutali, kumaiko onse kumene mudawaingira, chifukwa cha kulakwa kwao anakulakwirani nako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa