Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 22:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo adzayankha, Chifukwa anasiya pangano la Yehova Mulungu wao, ndi kugwadira milungu ina, ndi kuitumikira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo adzayankha, Chifukwa anasiya pangano la Yehova Mulungu wao, ndi kugwadira milungu ina, ndi kuitumikira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Nchifukwa chakuti anthu akewo adasiya chipangano chimene adapangana ndi Chauta, Mulungu wao. Adayamba kupembedza milungu ina ndi kumaitumikira.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndipo yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Chifukwa anasiya pangano limene anapangana ndi Yehova Mulungu wawo ndipo anapembedza ndi kutumikira milungu ina.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:9
16 Mawu Ofanana  

Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali ino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero chifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba ino?


popeza anandisiya Ine, nafukizira zonunkhira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake mkwiyo wanga udzayakira malo ano wosazimikanso.


chifukwa anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake ukali wanga utsanulidwa pamalo pano wosazimika.


Abwerera kuchitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu ina kuti aitumikire; nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao.


ndi kunena kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Aisraele: Wotembereredwa ndi munthu wosamvera mau a pangano ili,


Pamenepo uziti kwa iwo, Chifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu ina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga chilamulo changa;


Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitipalamula mlandu, chifukwa iwo anachimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, chiyembekezo cha atate ao.


Ndipo Yehova ati, Chifukwa asiya chilamulo changa ndinachiika pamaso pao, ndipo sanamvere mau anga, osayenda m'menemo;


Koma ndidzawasiya owerengeka apulumuke lupanga, ndi njala, ndi mliri, kuti afotokoze zonyansa zao kwa amitundu kumene afikako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zochita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazichite kopanda chifukwa zonse ndinazichita momwemo, ati Ambuye Yehova.


Ndipo amitundu adzadziwa kuti nyumba ya Israele idalowa undende chifukwa cha mphulupulu zao, popeza anandilakwira Ine; ndipo ndinawabisira nkhope yanga; m'mwemo ndinawapereka m'dzanja la adani ao, nagwa iwo onse ndi lupanga.


Momwemo chidzakhala chotonza ndi mnyozo, chilangizo ndi chodabwitsa kwa amitundu akukuzinga, pamene ndikuchitira maweruzo mu mkwiyo ndi ukali ndi madzudzulo aukali; Ine Yehova ndanena.


inde amitundu onse adzati, Yehova anachitira dziko ili chotero chifukwa ninji? Nchiyani kupsa mtima kwakukulu kumene?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa