Yeremiya 20:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo Pasuri anampanda Yeremiya mneneriyo, namuika matangadza amene anali mu Chipata cha Benjamini cha kumtunda, chimene chinali kunyumba ya Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo Pasuri anampanda Yeremiya mneneriyo, namuika matangadza amene anali m'chipata cha kumtunda cha Benjamini, chimene chinali kunyumba ya Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Tsono Pasuri adalamula kuti anthu amenye mneneri Yeremiya ndi kumuika m'ndende ku chipata cha Benjamini, ku Nyumba ya Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Tsono iye analamula kuti mneneri Yeremiyayo amenyedwe ndi kuyikidwa mʼndende pa Chipata chakumtunda kwa Benjamini ku Nyumba ya Yehova. Onani mutuwo |
Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga chidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwake, kuyambira ku Chipata cha Benjamini kufikira ku malo a chipata choyamba, kufikira ku Chipata cha Kungodya, ndi kuyambira Nsanja ya Hananele kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu.