Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 20:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo panali m'mawa mwake, kuti Pasuri anatulutsa Yeremiya m'matangadzamo. Ndipo Yeremiya anati kwa iye, Yehova sanatche dzina lako Pasuri, koma Magorimisabibu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo panali m'mawa mwake, kuti Pasuri anatulutsa Yeremiya m'matangadzamo. Ndipo Yeremiya anati kwa iye, Yehova sanatche dzina lako Pasuri, koma Magorimisabibu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 M'maŵa mwake Pasuri adatulutsa Yeremiya m'ndende, ndipo Yeremiya adauza Pasuri kuti, “Chauta sakutchulanso dzina loti Pasuri, koma loti ‘Zoopsa pa mbali zonse.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mmawa mwake, Pasuri anatulutsa Yeremiya mʼndende, ndipo Yeremiyayo anamuwuza kuti, “Pasuri, Yehova sadzakutchulanso dzina lako kuti Pasuri koma Zoopsa pa Mbali Zonse.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 20:3
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usamutcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara.


Sudzatchedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; chifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu.


Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.


Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.


Ndipo ndinanka kwa mneneri wamkazi; ndipo iye anatenga pakati nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, Utche dzina lake, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza.


nutulukire kuchigwa cha mwana wake wa Hinomu, chimene chili pa khomo la Chipata cha Mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe;


chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova kuti pamalo pano sipadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wake wa Hinomu, koma Chigwa Chophera anthu.


Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.


Ndipo Zefaniya wansembe anawerenga kalata amene m'makutu a Yeremiya mneneri.


Chifukwa chanji ndachiona? Aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osacheukira m'mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.


Usatulukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse.


Chifukwa chake, taonani, masiku alikudza, ati Yehova, ndipo sadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wa Hinomu, koma Chigwa cha Kuphera; pakuti adzataya mu Tofeti, kufikira malo akuikamo adzasowa.


Mwaitana zondiopsa mozungulira ngati tsiku la msonkhano; panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova; omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza.


Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pake, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israele; kapena kulowa m'dziko la Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.


nawatulutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa