Yeremiya 2:18 - Buku Lopatulika18 Tsopano uli nacho chiyani m'njira ya ku Ejipito, kumwa madzi a mtsinje wa Nailo? Uli nacho chiyani m'njira ya ku Asiriya, kumwa madzi a mtsinje wa Yufurate? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Tsopano uli nacho chiyani m'njira ya ku Ejipito, kumwa madzi a Sihori? Uli nacho chiyani m'njira ya ku Asiriya, kumwa madzi a m'mtsinje? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Nanga tsopano mudzapindulanji mukadzapita ku Ejipito, kukamwa madzi a m'Nailo? Mudzapeza phindu lanji mukadzapita ku Asiriya kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Tsopano mudzapindula chiyani mukapita ku Igupto, kukamwa madzi a mu Sihori? Ndipo mudzapindulanji mukapita ku Asiriya, kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate? Onani mutuwo |