Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 2:16 - Buku Lopatulika

16 Ananso a Nofi ndi a Tapanesi, anaswa pakati pamutu pako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ananso a Nofi ndi a Tapanesi, anaswa pakati pamtu pako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Aejipito a ku Memfisi ndi a ku Tapanesi akuphwanyani mitu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ndiponso Aigupto a ku Mefisi ndi a ku Tapanesi akuphwanyani mitu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:16
17 Mawu Ofanana  

Taona tsono ukhulupirira ndodo ya bango ili lothyoka, ndilo Ejipito; ndilo munthu akatsamirapo lidzampyoza dzanja lake; atero Farao mfumu ya Aejipito kwa onse omkhulupirira iye.


Ndipo Farao Neko anammanga mu Ribula, m'dziko la Hamati; kuti asachite ufumu mu Yerusalemu; nasonkhetsa dzikoli msonkho wa matalente zana limodzi la siliva, ndi talente limodzi la golide.


Akalonga a Zowani apusa, akalonga a Nofi anyengedwa; iwo asocheretsa Ejipito, amene ali mwala wa pangodya wa mafuko ake.


ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu; kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga otuluka mumtima.


Ndipo iye adzapitapita kulowa mu Yuda; adzasefukira, napitirira; adzafikira m'khosi; ndi kutambasula kwa mapiko ake, kudzakwanira dziko lanu m'chitando mwake, inu Imanuele.


Mau amene anadza kwa Yeremiya onena za Ayuda onse amene anakhala m'dziko la Ejipito, okhala pa Migidoli, ndi pa Tapanesi, ndi pa Nofi, ndi m'dziko la Patirosi, akuti,


Nenani mu Ejipito, lalikirani mu Migidoli, lalikirani mu Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.


Mwana wamkazi iwe wokhala mu Ejipito, dzikonzere kunka kundende; pakuti Nofi adzakhala bwinja, nadzapsa, mulibenso wokhalamo.


Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka mu Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamutu pa ana a phokoso.


Atero Ambuye Yehova, Ndidzaononganso mafano, ndi kuleketsa milungu yopanda pake ku Nofu; ndipo sadzaonekanso kalonga wochokera ku Ejipito, ndipo ndidzaopsa dziko la Ejipito.


Ndipo ndidzaika moto mu Ejipito; Sini adzamva kuwawa kwakukulu, ndi No adzagawika pakati, ndi Nofu adzaona adani usana.


Pakuti taonani, anachokera chionongeko, koma Ejipito adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao.


Ndi za Gadi anati, Wodala iye amene akuza Gadi; akhala ngati mkango waukazi, namwetula dzanja, ndi pakati pamutu pomwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa