Yeremiya 2:15 - Buku Lopatulika15 Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lake, mizinda yake yatenthedwa, mulibenso wokhalamo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lake, midzi yake yatenthedwa, mulibenso wokhalamo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Anthu a mitundu ina ambangulira ndi kumuwopsa ngati mikango. Dziko lake alisandutsa chipululu. Mizinda yake adaiwononga, idasanduka mabwinja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Adani ake abangulira ndi kumuopseza ngati mikango. Dziko lake analisandutsa bwinja; mizinda yake anayitentha popanda wokhalamo. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.