Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 2:10 - Buku Lopatulika

10 Pakuti pitani ku zisumbu za Kitimu nimuone; tumizani ku Kedara nimulingalire bwino; nimuone ngati chinalipo chotere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pakuti pitani ku zisumbu za Kitimu nimuone; tumizani ku Kedara nimulingalire bwino; nimuone ngati chinalipo chotere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pitani chakuzambwe, ku chilumba cha Kitimu, mukaone, tumani anthu chakuvuma, ku Kedara, akafufuze. Mudzaona kuti zoterezi sizidachitikepo nkale lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Pitani kumadzulo ku chilumba cha Kitimu, ndipo mukaone, tumizani anthu ku Kedara kuti akafufuze bwino; ndipo muona kuti zinthu zoterezi sizinachitikepo nʼkale lomwe:

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:10
21 Mawu Ofanana  

ndipo maina a ana a Ismaele, maina ao m'mibadwo yao ndi awa: woyamba wa Ismaele ndi Nebayoti; ndi Kedara, ndi Adibeele, ndi Mibisamu,


Ndipo anthu adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wao amene adatulutsa makolo ao m'dziko la Ejipito, natsata milungu ina, nailambira, naitumikira; chifukwa chake Yehova anawagwetsera choipa chonsechi.


Ndi ana a Yavani: Elisa, ndi Tarisisi, Kitimu, ndi Rodanimu.


Atakalamba tsono Davide ndi kuchuluka masiku, iye analonga mwana wake Solomoni akhale mfumu ya Israele.


Ana a Kohati: Amuramu, Izihara, Hebroni, ndi Uziyele; anai.


Tsoka ine, kuti ndili mlendo mu Meseki, kuti ndigonera m'mahema a Kedara!


Pakuti Ambuye anatero kwa ine, Chisanapite chaka malinga ndi zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wonse wa Kedara udzagoma;


Katundu wa Tiro. Kuwani, inu ngalawa za Tarisisi; chifukwa wapasudwa, kulibenso nyumba, kulibe polowera; kuchokera kudziko la Kitimu kwavumbulutsidwa kwa iwo.


Ndipo Iye anati, Iwe sudzakondwanso konse, iwe namwali wovutidwa, mwanawamkazi wa Sidoni; uka, oloka kunka ku Kitimu; ngakhale kumeneko iwe sudzapumai.


Za Kedara, ndi za maufumu a Hazori, amene anawakantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Yehova atero: Ukani, kwerani ku Kedara, funkhani ana a ku m'mawa.


Ndipo unatengako zovala zako, ndi kudzimangira misanje ya mawangamawanga, ndi kuchitapo chigololo; zotere sizinayenere kufika kapena kuchitika.


Arabiya ndi akalonga onse a ku Kedara anazolowerana nao malonda ako; anaankhosa, nkhosa zamphongo, ndi mbuzi, izi anagulana nawe.


Anasema nkhafi zako za thundu wa ku Basani, anapanga mipando yako yamnyanga, woika mu mtengo wanaphini wochokera ku zisumbu za Kitimu.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza kupokosera kwanu kwaposa kwa amitundu akukuzingani, ndipo simunayende m'malemba anga, kapena kuchita maweruzo anga, ngakhale maweruzo a amitundu akukuzingani simunawachite;


Pambuyo pake adzatembenuzira nkhope yake kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwake adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwake.


Pakuti zombo za ku Kitimu zidzafika kuyambana naye; chifukwa chake adzatenga nkhawa, nadzabwerera, nadzaipidwa mtima ndi chipangano chopatulika, nadzachita chifuniro chake; adzabweranso, nadzasamalira otaya chipangano chopatulika.


Koma zombo zidzafika kuchokera ku dooko la Kitimu, ndipo adzasautsa Asiriya, nadzasautsa Eberi, koma iyenso adzaonongeka.


Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati panu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.


Ndipo kunali kuti onse amene anachiona anati, Sichinachitika, inde sichinaoneke chotere chiyambire tsiku lokwera ana a Israele kutuluka m'dziko la Ejipito mpaka lero lino; lingiriranipo, mupangane nzeru, nimunene.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa