Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 19:3 - Buku Lopatulika

3 nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera malo ano choipa, chimene aliyense adzachimva, makutu ake adzachita woo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera malo ano choipa, chimene aliyense adzachimva, makutu ake adzachita woo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ukanene kuti, Inu mafumu a ku Yuda ndi onse okhala ku Yerusalemu, imvani mau a Chauta. Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, ‘Ndidzagwetsa tsoka loopsa pa malo ano, kotero kuti aliyense amene adzamve adzadzidzimuka kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ukanene kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu a ku Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti: Tamverani! Ine ndibweretsa mavuto pa malo pano mwakuti aliyense amene adzamve adzadzidzimuka.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 19:3
18 Mawu Ofanana  

Pamenepo amitundu adzaopa dzina la Yehova, ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu.


Ambuye padzanja lamanja lako adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake.


Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru; langikani, oweruza inu a dziko lapansi.


Nthawi zonse umapita, udzakutengani; chifukwa m'mawa ndi m'mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsa kokha, kumva mbiri yake.


Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.


ndipo uziti kwa iwo, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi Ayuda onse, ndi onse okhala mu Yerusalemu, amene alowa pa zipatazi;


Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu choipa, ndilingalira inu kanthu kakuchitira inu choipa; mubwerere tsono inu nonse, yense kunjira yake yoipa, nimukonze njira zanu ndi machitidwe anu.


Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera mzinda uwu ndi midzi yake yonse choipa chonse chimene ndaunenera; chifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga.


Pakuti, taonani, ndiyamba kuchita choipa pa mzinda umene utchedwa ndi dzina langa, kodi inu mudzakhala osalangidwa konse? Simudzakhala osalangidwa; pakuti ndidzaitana lupanga ligwe pa onse okhala m'dziko lapansi, ati Yehova wa makamu.


Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzafikitsa pa Yuda ndi pa onse okhala mu Yerusalemu choipa chonsecho ndawanenera iwo; chifukwa ndanena ndi iwo, koma sanamve; ndaitana, koma iwo sanandivomere.


chifukwa cha choipa chao anachichita kuutsa nacho mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu ina, imene sanaidziwe, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu.


Tamva, dziko lapansi iwe; taona, Ine ndidzatengera choipa pa anthu awa, chipatso cha maganizo ao, pakuti sanamvere mau anga, kapena chilamulo changa, koma wachikana.


Atero Yehova Mulungu, Choipa, choipa cha pa chokha, taona chilinkudza.


ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Taona, ndidzachita mwa Israele choliritsa mwini khutu kwa munthu yense wakuchimva.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa