Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 19:2 - Buku Lopatulika

2 nutulukire kuchigwa cha mwana wake wa Hinomu, chimene chili pa khomo la Chipata cha Mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 nutulukire kuchigwa cha mwana wake wa Hinomu, chimene chili pa khomo la chipata cha mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mupite ku Chigwa cha Benihinomu, pafupi pa Chipata cha Mapale. Kumeneko ukalengeze zimene ndikukuuza tsopano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 ndipo mupite ku Chigwa cha Hinomu chimene chili pafupi ndi pa chipata cha mapale. Pamenepo ukalengeze mawu amene ndikakuwuze.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 19:2
19 Mawu Ofanana  

Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'chigwa cha ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.


Nafukizanso yekha m'chigwa cha mwana wa Hinomu, napsereza ana ake m'moto, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israele.


Anapititsanso ana ake pamoto m'chigwa cha ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.


Potsatizana nao anakonza Zadoki mwana wa Imeri pandunji pa nyumba yake. Ndi potsatizana naye anakonza Semaya mwana wa Sekaniya, wosunga Chipata cha Kum'mawa.


Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Lalikira mau onsewa m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, kuti, Tamvani mau a pangano ili, ndi kuwachita.


Tauka, tatsikira kunyumba ya woumba, pamenepo ndidzakumvetsa mau anga.


Yehova atero: Ima m'bwalo la nyumba ya Yehova, ndi kunena kwa mizinda yonse ya Yuda, imene imadza kudzagwadira m'nyumba ya Yehova, mau onse amene ndikuuza iwe kuti unene kwa iwo; usasiyepo mau amodzi.


Pita; nulalikire mau awa kuyang'ana kumpoto, ndi kuti, Bwera iwe Israele wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang'anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndili wachifundo, ati Yehova, sindidzakhala nako kukwiya kunthawi zonse.


Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m'chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene sindinawauze, chimene sichinalowe m'mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.


Ima m'chipata cha nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova.


Nyamuka, pita ku Ninive mzinda waukulu uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.


Chimene ndikuuzani inu mumdima, tachinenani poyera; ndi chimene muchimva m'khutu, muchilalikire pa matsindwi a nyumba.


Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.


Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule mu Kachisi kwa anthu onse mau a Moyo umene.


nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa