Yeremiya 16:4 - Buku Lopatulika4 Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 onsewo adzafa ndi nthenda zoopsa. Sadzaŵalira maliro kapena kuŵaika m'manda. Adzakhala ngati ndoŵe yotayikira pansi. Ena adzafera pa nkhondo, ena adzafa ndi njala. Ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame ndi zilombo zakuthengo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 adzafa ndi nthenda zoopsa. Sadzawalira maliro kapena kuyikidwa mʼmanda koma adzakhala ngati ndowe zotayikira pansi. Ena adzaphedwa ku nkhondo ndipo ena adzafa ndi njala. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo.” Onani mutuwo |
Ndipo ndidzatenga otsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Ejipito akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Ejipito adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo.